Mkulu wina wa zaka 63 wadzinjata m’boma la Mzimba.

Mkuluyi amadziwika ndi dzina loti Davison Kumwenda ndipo amakhala m’dela la Mfumu yaikulu M’mbelwa ku Mzimba.

M’neneri wa polisi Peter Botha wanena kuti Kumwenda anachoka kunyumba kwake osatsanzika anthu apakhoma lake.

Ndipo masana wake bambo Kumwenda adawapeza atadzinjata mu mtengo wamango pafupi ndi nyumba yawo.

Botha adaonjezera ponena kuti Kumwena anali pa mkangano wa malo ndi anthu apachibale ndipo amfumu am’mudzimo amayendetsa nkhani ya malo.

Imfa ya bambo kumwenda yachitika patangotha masiku ochepa pomwe bambo wina wazaka 45 Josted Saka atadzinjataso m’boma la Mzimba.

 

 

(Visited 21 times, 1 visits today)


Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram