Mkazi wa malemu Professor Bingu wa Muthalika ‘Calista’ wati iye, sakukayika konse kuti ana amalemu Bingu, anabisa ‘Will’ yomwe mkuluyu analemba atakwatirana naye.

Calista wati, akukhulupilira zoti m’mene ankakondanirana ndi mwamuna wake, sangamusiye osamuyika pa will koma kuti achina Duwa ndiwomwe anataya will yi mwadala ndicholinga chofuna kumukhawulitsa.

Mayiyu wati, akamang’ala ku bwalo lamilandu kuti will yomwe ilipo panopayi, ikhale yopanda ntchito ndipo kuti, chuma cha Bingu, iyenso apeze nawo gawo ngati mkazi wake.

(Visited 16 times, 1 visits today)


Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram