Namatetule pa business m’dziko muno yemwenso ndi mkulu wa Mulli Brothers Limited (MBL) Leston Mulli, wadzudzula nduna yowona zachilungamo a Raph Kasambara kamba komukhokhomelera kuti asamapatsidwe contract inailiyonse yaboma.

Malingana ndi umboni omwe BNM yapeza, bambo Kasambara ndi amene analemba kalata ku mabungwe onse a boma mdziko muno chaka chatha yolamula kuti asadzayerekeze kuyipatsa contract company inailiyonse m’ma company 9 a Mulli ndipo kuti kutero, kuzasokoneza kafukufuku yemwe unduna wawo ukupanga pa milandu ina yomwe mkuluyu akumuganizila kuti anapalamula munthawi ya DPP.

Koma m’mawu ake Mulli wati iye, sakukayika konse kuti ndunayi ilinaye chifukwa ndipo wapempha a Kasambara kuti abwere poyera ndikunena vuto lomwe alinalo ndi iye.

(Visited 21 times, 1 visits today)


Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram