Amai awiri amwalira kamba kogwera mu gwembe ku  Dowa.

Apolisi atsimikiza zankhaniyi  ndipo azimai wa adziwika ndi maina awa Evelyn Lucas wazaka 38 ndi Namoyo Mwangeni wazaka 45 ndipo onsewa amachokera m’mudzi mwa Chiwere ku Dowa.

pakafukufuku wa apolisi ku Dowa, M’neneri wa Polisi Richard Mwayayoka Kaponda, wanena kuti imfa yadzidziyi inachitika pa 31 july, 2018 kwa kagwada dambo m’derali.

Poikilapo ndemanga Kaponda adati amai awiriwa adali ndi ana achichepere asanu ndi anayi pamene adapita ku dambo ku mtapo kotenga dothi lokonzera nyumba zawo.

ku damboko amakatenga dothi  ataona kuti dothilo linali patali azimaiwa adalowa ku gwembe kuti atape dothi lambiri mwachisoni atalowa ku gwembeko, gwembe lidagumuka ndikuwa phyinda amai awiri ndipo adafera pomwepo.

Anthu atadziwitsidwa za izi adayesetsa kufukula gwembero koma adapeza amaiwa atamwalira kale.

Maripoti ochokera kuchipatala atsimikiza za imfayi kuti azimaiwa adamwalira kamba ka dothi lomwe lidagumukira mkati  la gwembero.

(Visited 3 times, 1 visits today)
0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram