Wapampando wa bungwe lowona zachisankho la Malawi Electoral Commission Jane Ansah wati chisankho cha chaka cha mawa chidzachitika monga mwa zaka zonse za m’mbuyomu.

Izi zanenedwa pomwe bungweli likuchititsa kalembera wachisankho pogwiritsa njira yamakono yotchedwa Bio Metric.

Njirayi akuti ndiyachangu kwambiri pomwe anthu sakumatenga nthawi yayitali pomwe akufuna kulembetsa.

Kwa zaka zonse za mmbuyomu, anthu akhala akugwiritsa ntchito zikalata zomwe pamakhala nkhope za anthu womwe akupikisana nawo pachisankho.

Ansah wati ngakhale bungweli likuchititsa kalembera pogwiritsa ntchito ndondomeko zamakono kudzera mmakina apamwamba, anthu adzaponya voti yawo monga mwakale.

(Visited 9 times, 1 visits today)
0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram