Mkulu wina wazaka makumi anayi ndi ziwiri odziwika ndi dzina la Dickson Ulaya wamwalira kamba ka mowo wakachaso poti sadadye kalikonse.

M’neneri wa polisi ku Mangochi, Amina Tepani, wanena kuti izi zinachitika masana a lachitatu ku Matapwata Shabin ku Mangochi.

“Atangolandila ndalama za mwezi wa Sepitemba sabata lathali, mkuluyi wakhala asakupita ku ntchito ndipo iye wakhala akumwa Kachaso muma shabini osiyana siyana ku Mangochi” Amina adatero.

Dickson amagwira ntchito ku Agriculture ndipo amayang’anila ziweto.

Mkuluyi anakomoka atamwa mowa wambiri osadyera, kenako anthu achisoni adamutengela kuchipatala cha Mangochi.

Dickson amachokera ku Kambeta m’mudzi mwa mfumu yaikulu Mlumbe ku Zomba.

 

(Visited 32 times, 1 visits today)


Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram