Komiti ya nyumba ya malamulo yowona zamaphunziro yapempha sukulu za ukachenjede zaboma kuti ziyambe kupeza njira zopezera ndalama pazokha pofuna kupititsira patsogolo ntchito zawo.

Wapampando wakomitiyi, Dr. Elias Chakwera anena izi komitiyi itakayendera ku Chancellor College ku Zomba koma mwazina awuzidwa kuti sukuluyi, ikufunikira ndalama zokwana K5 billion pofika pa 1 March, 2018 zomwe zingaperewere chisanafike chaka chaboma pa 1 July monga zimakhalira zaka zonse.

Dr. Chakwera komabe analonjeza kuti ayesetsa kupempha boma kuti lithandize pavutoli kaamba kakuti ngati izi sizichitika mwansanga ndekuti sukuluyi itha kutsekedwa.

(Visited 3 times, 1 visits today)

0

Subscribe to our Youtube Channel :

Follow Us on Instagram