Ntembo wa yemwe anali mtsogoleri wa chipani cha United Independence (UIP) mayi Hellen Singh yemwe anapikisananawo pa chisankho cha patatu cha mchaka 2014 aliotcha mawa mu mzinda otchuka ndi malonda wa Blantyre.

Asante Masantche, m’modzi ku banja lofedwa wasimikiza za nkhaniyi yoyankhula ndi mtola nkhani wa faceofmalawi.

Malingana ndi Masantche, thupi la a Singh lizatengedwa ku nyumba yachisoni ya College of Medicine (CoM) kupita ku holo ya COMESA komwe anthu azakhale akukhudza thupi la a Singh ndikupitiliza ndimwambo wamapemphero asanapite ku gome la Sikh komwe akaliotche.

Mayi Singh amwalira loweluka ku chipatala cha Adventist atadwala nthenda ya cancer.

Malemu Singh anali katswiri pa malonda ndipo anali ndi kampani yobweleketsa magalimoto yomwe imatchedwa kuti SS Rent a Car.

Subscribe to our Youtube Channel: